3 Ndipo anakucepetsani, nakumvetsani odala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwa, angakhale makolo anu sanawadziwa; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakuturuka m'kamwa mwa Yehova.
4 Zobvala zanu sizinatha pathupi panu, phazi lanu silinatupa zaka izi makumi anai.
5 Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wace, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.
6 Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace, ndi kumuopa.
7 Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe, ndi la maiwe akuturuka m'zigwa, ndi m'mapiri;
8 dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uci;
9 dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yace nja citsulo, ndi m'mapiri ace mukumbe mkuwa.