1 Imvani Israyeli; mulikuoloka Yordano lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akuru ndi amphamvu akuposa inu, midzi yaikuru ndi ya malinga ofikira kuthambo,
2 anthu akuru ndi atalitali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?
3 Potero mudziwe lero lino, kuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene aoloka pamaso panu ngati moto wonyeketsa; iye adzawaononga, iye adzawagwetsa pamaso panu; potero mudzawapitikitsa, ndi kuwaononga msanga, monga Yehova analankhula ndi inu.
4 Musamanena mumtima mwanu, atawapitikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Cifukwa ca cilungamo canga Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapitikitsa pamaso panu cifukwa ca zoipa za amitundu awa.
5 Simulowa kulandira dziko lao cifukwa ca cilungamo canu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu cifukwa ca zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo.