13 Yehova ananenanso ndi ine, ndi kuti, Ndapenya anthu awa, taona, awa ndi anthu opulukira;
14 undileke, ndiwaononge, ndi kufafaniza dzina lao pansi pa thambo; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi waukuru woposa iwo.
15 Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a cipangano anali m'manja mwanga.
16 Ndipo ndinapenya, taonani, mudacimwira Yehova Mulungu wanu; mudadzipangira mwana wa ng'ombe woyenga; mudapatuka msanga m'njira imene Yehova adalamulira inu.
17 Pamenepo ndinagwira magome awiriwo, ndi kuwataya acoke m'manja anga awiri, ndi kuwaswa pamaso panu.
18 Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, cifukwa ca macimo anu onse mudacimwa, ndi kucita coipaco pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace.
19 Pakuti ndinacita mantha cifukwa ca mkwiyo waukali, umene Yehova anakwiya nao pa inu kukuonongani, Koma Yehova anandimvera nthawi ijanso.