8 Ndi pambuyo pace Ibzani wa ku Betelehemu anaweruza Israyeli.
9 Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu; ndi ana akazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ace amuna ana akazi makumi atatu ocokera kwina. Ndipo anaweruza Israyeli zaka zisanu ndi ziwiri.
10 Nafa Ibzani naikidwa ku Betelehemu.
11 Ndi pambuyo pace Eloni Mzebuloni anaweruza Israyeli; naweruza Israyeli zaka khumi.
12 Nafa Eloni Mzebuloni naikidwa m'Aijaloni m'dziko la Zebuloni.
13 Ndi pambuyo pace Abidonf mwana wa Hilele wa ku Piratoni anaweruza Israyeli.
14 Ndipo anali nao ana amuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a aburu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israyeli zaka zisanu ndi zitatu.