5 pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pace sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israyeli m'dzanja la Afilisti.
6 Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wace ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ace ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunsa uko acokera kapena sanandiuzanso dzina lace;
7 koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye ciri conse codetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire mpaka tsiku la kufa kwace.
8 Pamenepo Manowa anapembedza Yehova, nati, Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudamtumayo, natilangize ico tizicitira mwanayo akadzabadwa.
9 Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m'munda, mwanuna wace Manowa palibe.
10 Ndipo mkaziyo anafulumira nathamanga, nauza mwamuna wace, nanena naye, Taona, wandionekera munthu anandidzerayo tsiku lija.
11 Nanyamuka Manowa natsata mkazi wace, namdzera mwamuna uja, nanena naye, Kodi ndinu mwamuna ujamunalankhulandimkaziyu? Ndipo anati, Ndine amene.