1 Ndipo Samsoni anatsikira ku Timna, naona mkazi wa ku Timna wa ana akazi a Afilisti.
2 Nakwera iye, nauzaatatewacendi amai wace, nati, Ndapenya mkazi m'Timna wa ana akazi a Afilisti; ndipo tsono munditengere uyu akhale mkazi wanga.
3 Koma atate wace ndi amai wace ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana akazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samsoni kwa atate wace, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga.
4 Koma atate wace ndi amai wace sanadziwa kuti cidacokera kwa Yehova ici; popeza analikufuna kutola cifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israyeli.
5 Pamenepo anatsikira Samsoni, ndi atate wace ndi mai wace ku Timna, nadza ku minda yamphesa ya Timna; ndipo taona, mwana wa mkango wakomana naye namdzumira.