7 Ndipo Samsoni ananena nao, Mukatero ndidzakubwezerani cilango ndi pamenepo ndidzaleka.
8 Ndipo anawakantha nyung'unyu ndi ncafu, makanthidwe akuru; natsika nakhala m'phanga mwa thanthwe la ku Etamu.
9 Pamenepo Afilisti anakwera, namanga misasa m'Yuda, natandika m'Leki
10 Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera cifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samsoni, kumcitira iye monga anaticitira ife.
11 Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu, nati kwa Samsoni, Sudziwa kodi kuti Atilisti ndiwo akutilamulira ife? nciani ici waticitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandicitira ine ndawacitira iwo.
12 Ndipo ananena naye, Tatsika ife tikumange, kuti tikupereke m'dzanja la Atilisti. Nanena nao Samsoni, Mundilumbirire kuti simudzandigwera nokha.
13 Ndipo anati kwa iye, Iai, koma kumanga tidzakumanga, ndi kukupereka m'dzanja lao; koma kupha sitikupha iwe. Nammanga iye ndi zingwe ziwiri zatsopano, nakwera naye kucokera kuthanthwe.