18 Ndipo pamene Delila anaona kuti adamfotokozera mtima wace wonse, anatuma naitana akalonga a Afilisti, ndi kuti, Kwerani nthawi yino, pakuti wandifotokozera za mtima wace wonse. Nakwera akalonga a Afilisti nadza kwa iye nabwera nazo ndalamazo m'dzanja lao.