17 koma amuna asanu omukawo kukazonda dziko anakwera nalowako, natenga fano losema, ndi cobvala ca wansembe ndi timafano, ndi fano loyenga; ndi wansembe anaima polowera pa cipata pamodzi ndi amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida za nkhondo m'cuuno.
18 Atalowa iwo m'nyumba ya Mika, natengako fane losema, cobvala ca wansembe, ndi timafano, ndi fano loyenga, wansembeyo ananena nao, Mucitanji?
19 Ndipo ananena naye, Khala cete, tseka pakamwa pako, numuke nafe, nutikhalire atate ndi wansembe wathu; cikukomera nciti, kukhala wansembe wa nyumba ya munthu mmodzi, kapena kukhala wansembe wa pfuko ndi banja m'Israyeli?
20 Nukondwera mtima wa wansembeyo, natenga iye cobvala ca wansembe, ndi timafano ndi fano losema, nalowa pakati pa anthu.
21 Atatero anabwerera, nacoka, natsogoza ana ang'ono ndi zoweta ndi akatundu.
22 Atafika kutari ndi nyumba ya Mika, Mikayo anawamemeza amuna a m'nyumba zoyandikizana ndi yace, natsata ndi kuwapeza ana a Dani.
23 Ndipo anapfuula kwa ana a Dani. Naceuka iwo nati kwa Mika, Cakusowa ciani, kuti wamemeza anthu ako?