3 Pokhala iwo m'nyumba ya Mika, anazindikira mau a mnyamata Mleviyo, napambukirako, nanena naye, Anadza nawe kuno ndani? ucitanji muno? ukhala naco ciani kuno?
4 Ndipo ananena nao, Mika anandicitira cakuti cakuti, napangana nane za nchito, ndipo ndikhala wansembe wace.
5 Pamenepo ananena naye, Utifunsire kwa Mulungu, kuti tidziwe ngati ulendo wathu timukawo udzakoma.
6 Nanena nao wansembeyo, Mukani mumtendere, ulendo wanu muyendawo uli pamaso pa Yehova.
7 Pamenepo amuna asanuwa anacoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m'mwemo, kuti anakhalaokhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m'dzikomo munalibe mwini bwalo wakudtitsa manyazi m'cinthu ciri conse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu ali yense.
8 Ndipo asanuwo anafikanso kwa abale ao ku Zora ndi Esitaoli; ndi abale ao ananena nao, Mutani inu?
9 Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli cete kodi? musamacita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo,