26 Nadza mkaziyo kutaca, nagwa pakhomo pa nyumba ya munthu padali mbuye wace, kufikira kutayera.
27 Pamene mbuye wace anauka mamawa, natsegula pakhomo pa nyumba, naturuka kumka ulendo wace, taona, mkazi wace wamng'onoyo, atagwa pakhomo pa nyumba ndi manja ace paciundo.
28 Ndipo ananena naye, Tauka, timuke; koma panalibe womyankha. Pamenepo anamuika pa buru; nanyamuka mwamunayo, namka kwao.
29 Ndipo pofika iye kunyumba kwace, anatenga mpeni, nagwira mkazi wace wamng'onoyo namgawa ciwalo ciwalo magawo khumi ndi awiri, namtumiza ku mame onse a Israyeli.
30 Ndipo kunali kuti onse amene anaciona anati, Sicinacitika, inde sicinaoneka cotere ciyambire tsiku lokwera ana a Israyeli kuturuka m'dziko la Aigupto mpaka lero lino; lingiriranipo, mupangane nzeru, nimunene.