9 Pamenepo munthuyo ananyamuka kucoka, iye ndi mkazi wace wamng'ono ndi mnyamata wace; koma mpongozi wace, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kumka ulendo wanu kwanu.
10 Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nacoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwo Yerusalemu); ndi pamodzi naye panali aburu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wace wamng'ono.
11 Pofika iwo pa Yebusi linalimkulowa dzuwa, ndi mnyamata anati kwa mbuye wace, Tiyeni, tipambukire mudzi uwu wa Ayebusi ndi kugona pomwepa.
12 Koma mbuye wace ananena naye, Tisapambukire mudzi wacilendo, wosati wa ana a lsrayeli, koma tipitirire kumka ku Gibeya,
13 Nati kwa mnyamata wace, Tiyeni, tiyandikire kwinako: tigone m'Gibeya, kapena m'Rama.
14 Napitiriraiwo, nayenda, ndi dzuwa linawalowera pafupi pa Gibeya, ndiwo wa Benjamini.
15 Napambukirako, kuti alowe nagone ku Gibeya; nalowa iye, nakhala pansi m'khwalala la mudziwo, pakuti panalibe wina wowalandira m'nyumba agonemo, wakuwapatsa pogona.