11 Ndipo cimene mukacite ndi ici: mukaononge konse mwamuna ali yense, ndi mkazi ali yense wodziwa mwamuna mogona naye.
12 Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-gileadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.
13 Ndipo msonkhano wonse unatumiza mau kwa ana a Benjamini okhala m'thanthwe la Rimoni, nawalalikira mtendere.
14 Nakwera Abenjamini nthawi ija, ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga amoyo mwa akazi a Yabesi-gileadi; koma sanawafikira.
15 Ndipo anthu anamva cifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang'amba mapfuko a Israyeli.
16 Pamenepo akuru a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti m'Benjamini?
17 Nati iwo, Pakhale colowa ca iwo opulumuka a Benjamini, lingafafanizidwe pfuko m'Israyeli.