15 Ndipo anthu anamva cifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang'amba mapfuko a Israyeli.
16 Pamenepo akuru a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti m'Benjamini?
17 Nati iwo, Pakhale colowa ca iwo opulumuka a Benjamini, lingafafanizidwe pfuko m'Israyeli.
18 Koma sitikhoza ife kuwapatsa ana athu akazi akhale akazi ao; pakuti ana a Israyeli adalumbira ndi kuti, Atembereredwe wakupatsa Abenjamini mkazi.
19 Natiiwo, Taonani, pali madyerero a Yehova caka ndi caka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Beteli, kum'mawa kwa mseu wokwera kucokera ku Beteli kumka ku Sekemu, ndi kumwela kwa Lebona.
20 Ndipo analamulira ana a Benjamini ndi kuti, Mukani, mulalire m'minda yamphesa;
21 nimuyang'ane, ndipo taonani, ataturuka ana akazi a Silo kubvinabvina, pamenepo muturuke m'minda yamphesa ndi kudzigwirira yense mkazi wace mwa ana akazi a Silo, ndi kumuka naye ku dziko la Benjamini.