16 Ndipo Ehudi anadzisulira lupanga lakuthwa konse konse utali wace mkono; nalimangirira pansi pa zobvala zace pa ncafu ya kulamanja.
17 Ndipo anapereka mtulo kwa Egiloni, mfumu ya Moabu; koma Egiloni ndiye munthu wonenepa ndithu.
18 Ndipo atatha kupereka mtulowo, anauza anthu onyamula mtulo acoke.
19 Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndiri nao mau acinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani cete. Ndipo anaturuka onse akuimapo.
20 Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'cipinda cosanja copitidwa mphepo, Nati Ehudi, Ndiri nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wace.
21 Ndipo Ehudi anaturutsa dzanja lace lamanzere nagwira lupanga ku ncafu ya kulamanja nampyoza m'mimba mwace;
22 ndi cigumbu cace cinalowa kutsata mpeni wace; ndi mafuta anaphimba mpeniwo, pakuti sanasolola lupanga m'mimba mwace; nilituruka kumbuyo.