20 Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'cipinda cosanja copitidwa mphepo, Nati Ehudi, Ndiri nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wace.
21 Ndipo Ehudi anaturutsa dzanja lace lamanzere nagwira lupanga ku ncafu ya kulamanja nampyoza m'mimba mwace;
22 ndi cigumbu cace cinalowa kutsata mpeni wace; ndi mafuta anaphimba mpeniwo, pakuti sanasolola lupanga m'mimba mwace; nilituruka kumbuyo.
23 Pamenepo Ehudi anaturuka kukhonde namtsekera pamakomo pa cipinda cosanja nafungulira.
24 Ndipo ataturuka iye, anadza aka polo ace; napenya, ndipo taonani pamakomo pa cipinda cosanja mpofungulira; nati iwo, Angophimba mapazi m'cipinda cace cosanja copitidwa mphepo.
25 Ndipo analindirira mpaka anacita manyazi; koma taonani, sanatsegula pamakomo pa cipinda cosanja. Pamenepo anatenga mfungulo natsegula; ndipo taonani, mbuye wao wagwa pansi, wafa.
26 Ndipo Ehudi anapulumuka pakucedwa iwo, napitirira pa mafano osema, napulumuka kufikira Seira.