23 Pamenepo Ehudi anaturuka kukhonde namtsekera pamakomo pa cipinda cosanja nafungulira.
24 Ndipo ataturuka iye, anadza aka polo ace; napenya, ndipo taonani pamakomo pa cipinda cosanja mpofungulira; nati iwo, Angophimba mapazi m'cipinda cace cosanja copitidwa mphepo.
25 Ndipo analindirira mpaka anacita manyazi; koma taonani, sanatsegula pamakomo pa cipinda cosanja. Pamenepo anatenga mfungulo natsegula; ndipo taonani, mbuye wao wagwa pansi, wafa.
26 Ndipo Ehudi anapulumuka pakucedwa iwo, napitirira pa mafano osema, napulumuka kufikira Seira.
27 Ndipo kunali, pakufika iye anaomba lipenga ku mapiri a Efraimu; ndi ana a Israyeli anatsika naye kucokera kumapiri, nawatsogolera iye.
28 Ndipo ananena nao, Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amoabu m'manja mwanu. Ndipo anatsika ndi kumtsata, natsekereza Amoabu madooko a Yordano, osalola mmodzi aoloke.
29 Ndipo anakantha Amoabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onsewa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuka ndi mmodzi yense.