3 anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebano, kuyambira phiri la Baalaherimoni mpaka polowera ku Hamati.
4 Amenewo anakhala coyesera Israyeli kuti Yehova adziwe ngati adzamvere malamulo ace, amene analamulira makolo ao mwa dzanja la Mose.
5 Ndipo ana a Israyeli anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi;
6 nakwatira ana akazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana amuna a iwowa natumikira milungu yao.
7 Ndipo ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wao, natumikira Abaala ndi zifanizo.
8 Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unayakira Israyeli ndipo anawagulitsa m'dzanja la KusaniRisataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israyeli anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu.
9 Ndipo pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israyeli mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyeli mwana wa'Kenazi, mng'ono wace wa Kalebe.