16 Wakhaliranji pakati pa makola,Kumvera kulira kwa zoweta?Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikuru.
17 Gileadi anakhala tsidya lija la Yordano;Ndi Dani, akhaliranji mzombo?Aseri anakhala pansi m'mphepete mwa nyanja,Nakhalitsa pa nyondo yace ya nyanja.
18 Zebuloni ndiwo anthu anataya moyo wao mpaka imfa,Nafitali yemwe poponyana pamisanje.
19 Anadza mafumu, nathira nkhondoPamen'epo anathira nkhondo mafumu a Kanani.M'Taanaki, ku madzi a Megido;Osatengako phindu la ndarama.
20 Nyenyezi zinathira nkhondo yocokera kumwamba,M'mipita mwao zinathirana ndi Sisera.
21 Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,Mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni.Yenda mwamphamvu, moyo wangawe.
22 Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda,Ndi kutumphatumpha, kurumphatumpha kwa anthu ace eni mphamvu,