3 Imvani mafumu inu; cherani makutu, akalonga inu;Ndidzayimbira ine Yehova, inetu;Ndidzamuyimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israyeli,
4 Yehova, muja mudaturuka m'Seiri,Muja mudayenda kucokera ku thengo la Edomu,Dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha,Inde mitambo inakha madzi.
5 Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova,Sinai ili pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israyeli.
6 Masiku a Samagara, mwana wa Anati,Masiku a Yaeli maulendo adalekekaNdi apanjira anayenda mopazapaza,
7 Miraga idalekeka m'Israyeli, idalekeka.Mpaka ndinauka ine Debora,Ndinauka ine amai wa Israyeli.
8 Anasankha milungu yatsopano,Pamenepo nkhondo inaoneka kuzipata.Ngati cikopa kapena nthungo zidaonekaMwa zikwi makumi anai a Israyeli?
9 Mtima wanga ubvomerezana nao olamulira a m'Israyeli,Amene anadzipereka mwaufulu mwaanthu.Lemekezani Yehova.