28 Ndipo pakuuka mamawa amuna a ku mudziwo, taonani, guwa la nsembe la Baala litagamuka, ndi cifanizo cinali pomwepo citalikhidwa ndi ng'ombe yaciwiri yoperekedwa pa guwa la nsembe adalimanga.
29 Nanenana wina ndi mnzace, Wacita ici ndani? Ndipo atafunafuna nafunsafunsa, anati, Gideoni, mwana wa Yoasi wacita ici.
30 Pamenepo amuna a ku mudziwo anati kwa Yoasi, Umturutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha cifanizo cinali pomwepo.
31 Koma Yoasi anati kwa onse akumuimirira, Kodi inu mumnenera Baala mlandu? Kapena kodi mudzampulumutsa iye? iye amene amnenera mlandu aphedwe kukali m'mawa; akakhala mulungu adzinenere yekha mlandu, popeza wina wamgamulira guwa lace la nsembe.
32 Cifukwa cace anamucha tsiku lija Yerubaala, ndi kuti, Amnenece mlandu Baala popeza anamgamulira guwa lace la nsembe.
33 Pamenepo Amidyani onse ndi Aamaleki ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'cigwa ca Yezreeli.
34 Koma mzimu wa Yehova unabvana Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abieziri analalikidwa kumtsata iye.