5 Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ali yense akapiza madzi pa lilime lace, monga akhatira garu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo ali yense agwada pakumwa.
6 Ndi kuwerenga kwa iwo akukhatira, ndi kuika dzanja lao kukamwa kwao, ndiko mazana atatu; koma ena onse anagwada pakumwa madzi.
7 Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidyani m'dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwace.
8 Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israyeli amuke, yense kuhema kwace; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midyani inali kunsi kwace m'cigwa.
9 Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako.
10 Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa;
11 nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wace ku cilekezero ca anthu azidaa m'misasa.