10 Zeba ndi Tsalimuna ndipo anali m'Karikori, ndi a m'misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum'mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga.
11 Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m'mahema kum'mawa kwa Noba, ndi Yogibea, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima.
12 Ndipo Zeba ndi Tsalimuna anathawa; koma anawatsata, nagwira mafumu awiri a Midyani Zeba ndi Tsalimuna, nanjenjemeretsa khamu lonse.
13 Pamenepo Gideoni mwana wa Yoasi anabwerera kunkhondo pokwerera pa Heresi.
14 Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ace amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri.
15 Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Tsalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?
16 Ndipo anagwira akulu, a m'mudzi ndi minga ya kucipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti.