17 pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wace, nakupulumutsani m'dzanja la Amidyani;
18 koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ace, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wace, akhale mfumu ya pa eni ace a ku Sekemu, cifukwa ali mbale wanu;
19 ngati tsono mwacitira Yerubaala ndi nyumba yace zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu;
20 koma ngati simunatero, uturuke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ace a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nuturuke mota kwa eni ace a ku Sekemu, ndi ku nyumba yace ya Milo, nunyeketse Abimeleki.
21 Pamenepo Yotamu anafulumira, nathawa, namuka ku Beeri, nakhala komweko, cifukwa ca Abimeleki mbale wace.
22 Abimeleki atakhala kalonga wa Israyeli zaka zitatu,
23 Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ace a ku Sekemu; ndi eni ace a ku Sekemu anamcitira Abimeleki mosakhulupirika;