29 Mwenzi anthu awa akadakhala m'dzanja langa; ndikadamcotsadi Abimeleki. Ndipo anati kwa Abimeleki, Curukitsa khamu lako, nuturuke.
30 Pamene Zebuli woyang'anira mudzi anamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, anapsa mtima.
31 Natuma mithenga kwa Abimeleki monyenga nati, Taonani Gaala ndi abale ace afika ku Sekemu; ndipo taonani, akupandukitsirani mudzi.
32 Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo;
33 ndipo kukhale kuti m'mawa, pakuturuka dzuwa, muuke mamawa mugwere mudziwo; ndipo taonani, akakuturukirani iye ndi anthu ali naye, uzimcitira monga lidziwa dzanja lako.
34 Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai.
35 Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anaturuka, naima polowera pa cipata ca mudzi; nauka Abimeleki ndi anthu anali naye m'molalira.