4 Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pace ndi opepuka amene anamtsata.
5 Ndipo anamuka ku nyumba ya atate wace ku Ofira, nawapha abale ace ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.
6 Pamenepo anasonkhana eni ace onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa coimiritsa ciri m'Sekemu.
7 Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu pa phiri la Gerizimu, nakweza mau ace, napfuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ace a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.
8 Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo waazitona, Ukhale iwe mfumu yathu.
9 Koma mtengo waazitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?
10 Pamenepo mitengo inati kwa mkuyu. Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.