42 Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti anthu anaturuka kumka kuminda; ndipo anauza Abimeleki.
43 Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m'minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkuturuka m'mudzi; nawaukira iye nawakantha.
44 Ndi Abimeleki ndi magulu okhala naye anathamanga naima polowera pa cipata ca mudzi; ndi magulu awiriwo anagwera onse okhala m'munda, nawakantha.
45 Ndipo Abimeleki analimbana ndi mudzi tsiku lija lonse; nalanda mudzi nawapha anthu anali m'mwemo; napasula mudzi; nawazapo mcere.
46 Ndipo pamene eni ace onse a nsanja ya ku Sekemu anacimva, analowa m'ngaka ya nyumba ya Eliberiti.
47 Ndipo anauza Abimeleki kuti amuna onse a nsanja ya ku Sekemu asonkhane.
48 Pamenepo Abimeleki anakwera kumka ku phiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lace Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kulika paphewa pace, nati kwa anthu okhala naye, Ici munaciona ndacita, fulumirani, mucite momwemo.