12 Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israyeli; ndipo anati pamaso pa Israyeli,Dzuwa iwe, linda, pa Gibeoni,Ndi Mwezi iwe, m'cigwa ca Aialo.
13 Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaimaMpaka anthu adabwezera cilango adani ao.Kodi ici sicilembedwa m'buku la Yasari? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.
14 Ndipo panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m'tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mau a munthu; pakuti Yehova anathirira Israyeli nkhondo.
15 Pamenepo Yoswa anabwerera, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye, ku cigono ca ku Giligala.
16 Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda,
17 Ndipo anauza Yoswa ndi kuti, Mafumu asanuwa apezeka obisala m'phanga la ku Makeda.
18 Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikuru kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge;