17 Ndipo anauza Yoswa ndi kuti, Mafumu asanuwa apezeka obisala m'phanga la ku Makeda.
18 Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikuru kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge;
19 koma inu musaime, pitikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'midzi mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu.
20 Ndipo kunali, Yoswa ndi ana a Israyeli atatha kuwakantha, makanthidwe akurukuru mpaka atatha psiti, ndipo otsala a iwo atalowa m'midzi ya malinga,
21 anthu onse anabwerera kucigono kwa Yoswa pa Makeda ndi mtendere. Palibe munthu anacitira cipongwe mmodzi yense wa ana a Israyeli.
22 Pamenepo Yoswa anati, Tsegula pakamwa pa phanga ndi kunditurutsira m'phanga mafumu asanuwo.
23 Ndipo anatero, naturutsira m'phanga mafumu asanuwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimutu, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni.