2 Sihoni mfumu ya Aaroori wokhala m'Hesiboni, wocita ufumu kuyambira ku Aroeri ndiwo m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi pakati pa cigwa ndi pa Gileadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;
3 ndi pacidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kucidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere kum'mawa, njira ya Beti-Yesimoti; ndi kumwela pansi pa matsikiro a Pisiga.
4 Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basana wotsala wa Arefai, wokhala ku Asitarotu ndi ku Edrei,
5 nacita ufumu m'phiri la Herimoni, ndi m'Saleka, ndi m'Basana lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Gileadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni.
6 Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israyeli anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi pfuko la Manase logawika pakati, likhale colowacao.
7 Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israyeli anawakantha tsidya lija la Yordano kumadzulo, kuyambira Baala-gadi m'cigwa ca Lebano mpaka phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mapfuko a Israyeli, likhale lao lao, monga mwa magawo ao;
8 kumapiri ndi kucigwa, ndi kucidikha, ndi kumatsikiro, ndi kucipululu, ndi kumwela: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi: