3 Pakuti Mose adapatsa mapfuko awiri, ndi pfuko logawika pakati, colowa tsidya ito la Yordano; koma sanapatsa Alevi colowa pakati pao,
4 Pakuti ana a Yosefe ndiwo mapfuko awiri, Manase ndi Efraimu; ndipo sanawagawira Alevi kanthu m'dziko, koma midzi yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi cuma cao.
5 Monga Yehova analamulira Mose, momwemo ana a Israyeli anacita, nagawana dziko.
6 Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa cimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu m'KadesiBarinea.
7 Ndinali ine wa zaka makumi anai muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kucokera ku Kadesi-Barinea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mau, monga momwe anakhala mumtima mwanga.
8 Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.
9 Ndipo Mose analumbira tsiku lomwelo ndi kuti, Zedi, dzikoli phazi lako lapondapo lidzakhala colowa cako, ndi ca ana ako kosalekeza, cifukwa unatsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.