4 Pakuti ana a Yosefe ndiwo mapfuko awiri, Manase ndi Efraimu; ndipo sanawagawira Alevi kanthu m'dziko, koma midzi yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi cuma cao.
5 Monga Yehova analamulira Mose, momwemo ana a Israyeli anacita, nagawana dziko.
6 Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa cimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu m'KadesiBarinea.
7 Ndinali ine wa zaka makumi anai muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kucokera ku Kadesi-Barinea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mau, monga momwe anakhala mumtima mwanga.
8 Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.
9 Ndipo Mose analumbira tsiku lomwelo ndi kuti, Zedi, dzikoli phazi lako lapondapo lidzakhala colowa cako, ndi ca ana ako kosalekeza, cifukwa unatsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.
10 Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi mak umi anai ndi zisanu kuyambira nthawi ija Yehova ananena kwa Mose mau awa, poyenda Israyeli m'cipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lero lino.