1 Ndipo maere aciwiri anamturukira Simeoni, pfuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi colowa cao cinali pakati pa colowa ca ana a Yuda.
2 Ndipo anali naco colowa cao Beeri-seba, kapena Seba, ndi Molada;
3 ndi Hazarasuala, ndi Bala, ndi Ezemu;
4 ndi Elitoladi, ndi Betuli, ndi Horimu;
5 ndi Zikilaga, ndi Beti-malikabotu, ndi Hazari-susa:
6 ndi Beti-lebaotu, ndi Saruheni; midzi khumi ndi itatu ndi miraga yao;
7 Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asana; midzi inai ndi miraga yao;