15 ndi Kata, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi miraga yao.
16 Ici ndi colowa ca ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miraga yao.
17 Maere acinai anamturukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao.
18 Ndi malire ao anali ku Yezireeli, ndi Kesulotu, ndi Sunemu;
19 ndi Hafaraimu, ndi Sioni, ndi Anaharati;
20 ndi Rabiti ndi Kisioni, ndi Ebezi;
21 ndi Remeti ndi Eni-ganaimu ndi Eni-hada, ndi Beti-Pazezi;