26 ndi Alameleki, ndi Amadi, ndi Misali; nafikira ku Karimeli kumadzulo ndi ku Sihorilibinati;
27 nazungulira koturukira dzuwa ku Beti-dagoni, nafikira ku Zebuloni ndi ku cigwa ca Ifita-eli, kumpoto ku Beti-emeki, ndi Nehieli; naturukira ku Kabulu kulamanzere,
28 ndi Ebroni, ndi Rehobo, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkuru;
29 nazungulira malice kumka ku Rama, ndi ku mudzi wa linga la Turo; nazungulira malire kumka ku Hosa; ndi maturukiro ace anali kunyanja, kucokera ku Hebeli mpaka ku Akizibu;
30 Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobo; midzi makumi awiri mphambu iwiri ndi miraga yao,
31 Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Aseri monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miragayao.
32 Maere acisanu ndi cimodzi anaturukira ana a Nafitali, ana a Nafitali monga mwa mabanja ao.