30 Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobo; midzi makumi awiri mphambu iwiri ndi miraga yao,
31 Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Aseri monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miragayao.
32 Maere acisanu ndi cimodzi anaturukira ana a Nafitali, ana a Nafitali monga mwa mabanja ao.
33 Ndipo malire ao anayambira ku Helefi, ku thundu wa ku Zaanani, ndi Adaminekebi, ndi Yabineeli, mpaka ku Lakumu; ndi maturukiro ace anali ku Yordano;
34 nazungulira malire kumka kumadzulo ku Azinotu-tabori, naturukira komweko kumka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Aseri kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordano kum'mawa.
35 Ndipo midzi yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti;
36 ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori;