33 Ndipo malire ao anayambira ku Helefi, ku thundu wa ku Zaanani, ndi Adaminekebi, ndi Yabineeli, mpaka ku Lakumu; ndi maturukiro ace anali ku Yordano;
34 nazungulira malire kumka kumadzulo ku Azinotu-tabori, naturukira komweko kumka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Aseri kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordano kum'mawa.
35 Ndipo midzi yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti;
36 ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori;
37 ndi Kedesi, ndi Edrei, ndi Eni-hazori;
38 ndi Ironi, ndi Migidala-eli, Horemu, ndi Betianati, ndi Beti-semesi; midzi khumi ndi isanu ndi inai, ndi miraga yao.
39 Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Nafitali, monga mwa mabanja ao, midzi ndi miraga yao.