36 ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori;
37 ndi Kedesi, ndi Edrei, ndi Eni-hazori;
38 ndi Ironi, ndi Migidala-eli, Horemu, ndi Betianati, ndi Beti-semesi; midzi khumi ndi isanu ndi inai, ndi miraga yao.
39 Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Nafitali, monga mwa mabanja ao, midzi ndi miraga yao.
40 Maere acisanu ndi ciwiri anaturukira pfuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao.
41 Ndipo malire a colowa cao anali Zora, ndi Esitaoli ndi Iri-semesi;
42 Saalabini, ndi Aijaloni ndi ltila;