39 Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Nafitali, monga mwa mabanja ao, midzi ndi miraga yao.
40 Maere acisanu ndi ciwiri anaturukira pfuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao.
41 Ndipo malire a colowa cao anali Zora, ndi Esitaoli ndi Iri-semesi;
42 Saalabini, ndi Aijaloni ndi ltila;
43 ndi Eloni ndi Timna ndi Ekroni;
44 ndi Eliteke, ndi Gibetoni, ndi Baalati;
45 ndi Yehudi, ndi Bene-beraki, ndi Gatirimoni;