45 ndi Yehudi, ndi Bene-beraki, ndi Gatirimoni;
46 ndi Me-jarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pajapo.
47 Koma malire a ana a Dani anaturuka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, naucha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao.
48 Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miraga yao.
49 Ndipo atatha kuligawa dziko likhale colowa cao monga mwa malire ace, ana a Israyeli anapatsa Yoswa mwana wa Nuni colowa pakati pao;
50 monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mudzi umene anawapempha, ndiwo Timinatisera, ku mapiri a Efraimu; ndipo anamangamudziwonakhala m'mwemo.
51 Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazare wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli, zikhale zao zao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la cihema cokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.