32 Ndipo motapira pa pfuko la Nafitali, Kedesi m'Galileya ndi mabusa ace, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo, ndi Hamotidori ndi mabusa ace, ndi Karitani ndi mabusa ace, midzi itatu.
33 Midzi yonse ya Agerisoni monga mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu ndi mabusa ao.
34 Ndipo anapatsa kwa mabanja a ana a Merari, otsala a Alevi, motapira pa pfuko la Zebuloni, Yokineamu ndi mabusa ace, ndi Karita ndi mabusa ace,
35 Dimna ndi mabusa ace, Nahalala ndi mabusa ace; midzi inai.
36 Ndipo motapira pa pfuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ace, ndi Yahazi ndi mabusa ace,
37 Kedimotu ndi mabusa ace, ndi Mefati ndi mabusa ace; midzi inai.
38 Ndipo motapira m'pfuko la Gadi, Ramoti m'Gileadi ndi mabusa ace ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ace;