7 Ndipo gawo limodzi la pfuko la Manase, Mose anawapatsa colowa m'Basana; koma gawo lina Yoswa anawaninkha colowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordano kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;
8 nanena nao ndi kuti, Bwererani naco cuma cambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndi siliva, ndi golidi, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi maraya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.
9 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anabwerera, nacoka kwa ana a Israyeli ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kumka ku dziko la Gileadi, ku dziko lao lao, limene anakhala eni ace, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.
10 Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordano, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga ku Yordano guwa la nsembe, guwa lalikuru maonekedwe ace.
11 Ndipo ana a Israyeli anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga guwa la nsembe pandunji pa dziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordano, ku mbali ya ana a Israyeli.
12 Pamene ana a Israyeli anamva ici msonkhano wonse wa ana a Israyeli anasonkhana ku Silo, kuti awakwerere kuwathira nkhondo.
13 Ndipo ana a Israyeli anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Gileadi, Pinehasi mwana wa Eleazare wansembe,