9 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anabwerera, nacoka kwa ana a Israyeli ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kumka ku dziko la Gileadi, ku dziko lao lao, limene anakhala eni ace, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.
10 Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordano, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga ku Yordano guwa la nsembe, guwa lalikuru maonekedwe ace.
11 Ndipo ana a Israyeli anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga guwa la nsembe pandunji pa dziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordano, ku mbali ya ana a Israyeli.
12 Pamene ana a Israyeli anamva ici msonkhano wonse wa ana a Israyeli anasonkhana ku Silo, kuti awakwerere kuwathira nkhondo.
13 Ndipo ana a Israyeli anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Gileadi, Pinehasi mwana wa Eleazare wansembe,
14 ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mapfuko onse a Israyeli; yense wa iwowa ndiye mkuru wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israyeli.
15 M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Gileadi, ananena nao ndi kuti,