11 Taonani, likasa la cipangano La Ambuye wa dziko lonse lapansi lioloka Yordano pamaso panu,
12 Ndipo tsono, mudzitengere amuna khumi ndi awiri mwa mapfuko a Israyeli, pfuko limodzi mwamuna mmodzi.
13 Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m'madzi a Yordano, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ocokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi.
14 Ndipo kunali pocoka anthu ku mahema ao kukaoloka Yordano, ansembe anasenza likasa la cipangano pamaso pa anthu.
15 Ndipo pamene iwo akusenza likasa anafika ku Yordano, nathibika m'mphepete mwa madzi mapazi a ansembe akusenza likasa, pakuti Yordano asefuka m'magombe ace onse, nyengo yonse ya masika,
16 pamenepo madzi ocokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adamu, ndiwo mudzi wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kumka ku nyanja ya cidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.
17 Ndipo ansembe akulisenza likasa la cipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordano, ndi Aisrayeli onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordano.