6 Pakuti ana a Israyeli anayenda m'cipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo oturuka m'Aigupto udatha, cifukwa ca kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci.