1 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ace ndi mudzi wace ndi dziko lace;
2 ndipo uzimcitira Ai ndi mfumu yace monga umo unamcitira Yeriko ndi mfumu yace; koma zofunkha zace ndi ng'ombe zace mudzifunkhire nokha; udziikire anthu aja lire kukhonde kwa mudzi.
3 Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,
4 nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mudzi; musakhalira kutali ndi mudzi, koma mukhale okonzekeratu nonse;