6 Ndipo mkazi anathawira kucipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku cikwi cimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.
7 Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikayeli ndi angelo ace akucita nkhondo ndi cinjoka; cinjokanso ndi angelo ace cinacita nkhondo;
8 ndipo sicinalakika, ndipo sanapezekanso malo ao m'mwamba.
9 Ndipo cinaponyedwa pansi cinjoka cacikuru, njoka yokalambayo, iye wochedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; cinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ace anaponyedwa naye pamodzi.
10 Ndipo ndinamva mau akuru m'Mwamba, nanena, Tsopano zafika cipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wace; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.
11 Ndipo iwo anamlaka iye cifukwa ca mwazi wa Mwanawankhosa, ndi cifukwa ca mau a umboni wao; ndipo sanakonda moyo wao kungakhale kufikira imfa.
12 Cifukwa cace, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, cifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukuru, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.