5 Ndipo zitatha izi ndinaona, ndipo panatseguka pa Kacisi wa cihema ca umboni m'Mwamba:
6 Ndipo anaturuka m'Kacisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atabvala mwala woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolidi pacifuwa pao,
7 Ndipo cimodzi ca zamoyo zinai cinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolidi zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.
8 Ndipo Kacisi anadzazidwa ndi utsi wocokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yace; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa m'Kacisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.