1 Zitatha izi ndinaona mngelo wina wakutsika m'Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukuru; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wace.
2 Ndipo anapfuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babulo waukuru, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.
3 Cifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa cigololo cace mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anacita naye cigololo; ndipo ocita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyererakwace.
4 Ndipo ndinamva mau ena ocokera Kumwamba, nanena, Turukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi macimo ace, ndi kuti mungalandireko ya miliri yace;
5 pakuti macimo ace anaunjikizana kufikira m'Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zace.
6 Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa nchito zace; m'cikhomo unathiramo, muuthirire cowirikiza.