4 Ndipo ndinamva mau ena ocokera Kumwamba, nanena, Turukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi macimo ace, ndi kuti mungalandireko ya miliri yace;
5 pakuti macimo ace anaunjikizana kufikira m'Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zace.
6 Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa nchito zace; m'cikhomo unathiramo, muuthirire cowirikiza.
7 Monga momwe unadzicitira ulemu, nudyerera, momwemo muucitire eouzunza ndi couliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwace, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.
8 Cifukwa cace miliri yace idzadzam'tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; cifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.
9 Ndipo mafumu a dziko ocita cigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwace, poima patali,
10 cifukwa cakuopa cizunzo cace, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuruwo, Babulo, mudzi wolimba! pakuti m'ora limodzi cafika ciweruziro canu.